







(Wovumbulutsidwa ndi mneneri Kacou Philippe kwa Woyera mtima wa padziko lonse lapansi pa 28 februwale 2021).
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adalengeza pa 8 julayi 2021
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adalengeza pa 12 ogasiti 2021)
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adalengeza pa 7 novembala 2021)
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adawanena pa 12 februware 2022)
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adanena pa 17 epulo 2022
(Mawu amene mneneri Kacou Philippe adawanena pa 17 julaye 2022)
(Vumbulutso limene mneneri Kacou Philippe adapereka pa 9 okutobala 2022)
(Vumbulutso limene mneneri Kacou Philippe adapereka, pa 18 Dicembala 2022)
(Vumbulutso limene mneneri Kacou Philippe adapereka, pa 08 julaye 2023)
(Vumbulutso loperekedwa ndi mneneri Kacou Philippe pa 8 julaye wa 2023)
(Vumbulutso loperekedwa ndi mneneri Kacou Philippe pa 17 seputembala wa 2023)

Kacou Philippe adabadwa mu dicembala wa 1972 ku Katadji, mdera la Sikensi (Ivory Coast). Iye ndi mwana wa mlimi wosaphunzira. Atatha sukulu ya pulaimale, Kacou Philippe adangomaliza makalasi woyambirira anayi wa ku sekondale. Kuyambira 1992 mpaka 2002, iye adutsa nthawi yake yambiri ngati wantchito ku malo womanga.
Zonse zidayamba ndi masomphenya womwe iye adali nawo pa 24 epulo wa 1993. Choyamba, kudali kwa wansembe wa chikatolika kumene iye adapita kuti amvetse tanthauzo la masomphenyawo. Kenako, iye adapita kwa achibaptisti, ndi amene iye adakhala nawo kwa miyezi itatu, ndipo kenako iye akumana ndi gulu la William Branham, mlaliki wa ku America. Ndi gulu ili limene iye adakhalabe wotsatira wamba kuyambira 1993 mpaka 2002.
Kacou Philippe adayamba ndi maulaliki wake wa poyera mu julayi wa 2002, pambuyo pa kuyenderedwa kachiŵiri ndimngelo kumene iye adali nako mu 1993. Kacou Philippe akunenetsa kuti ndiye mneneri-wamthenga wa mfuu wa pakati pausiku, malingana ndi Mateyu 25:6.
Kwa Kacou Philippe, mipingo yonse ikutumikira mdierekezi mu dzina la Yesu Khristu. Iye amafotokoza nthawi zambiri masomphenya wena womwe iye adali nawo mu 1993, ndipo womwe iye akunena kuti adawona atsogoleri wa mipingo mwa mawonekedwe wachilendo: "Matupi wawo adali matupi a wanthu, koma mitu yawo idali mitu ya nyama zolekanalekana." Pamenepo, zidayamba zokambirana ndiponso mitsutsano yoyambirira.
Kacou Philippe amalalikira zinsinsi zambiri, monga izi: "Ngati Mulungu adawononga zoyipa zonse mu chigumula mu nthawi ya Nowa, nanga bwanji choipa chidapezedwabe pa dziko pambuyo pa chigumula?" Ndipo ulaliki umenewu ukufalitsidwa kwathunthu kudzera pa nsanja ya nkhani ya ku Cameroon. Kacou Philippe akunena kuti mawu wake ali ndi phindu lomwelo lolingana ndi mawu wa aneneri wa m'Baibulo.
Kwa Kacou Philippe, Mpingo ukuyamba ndi Yohane M’batizi ndipo ndi ubatizo wa kulapa. Kenako pakubwera ubatizo wa kuwomboledwa ku machimo ndi atumwi, kenako ubatizo wa kulungamitsa mwa chikhulupiriro ndi Martin Luther, kenako ubatizo wa kubadwanso kwa Mpingo pambuyo pa zizunzo zoyambirira za chiroma, kenako ubatizo wa kuvomerezedwa, kenako ubatizo wa kuyeretsa ndi John Wesley, kenako ubatizo wa kukonzedwanso ndi Chipentekoste, kenako ubatizo wa kubwezeretsanso ndi William Branham ndipo, pomaliza, ubatizo wa kubwezera ndi Kacou Philippe. Ndipo akunena kuti, kupatula izi, maubatizo wena wonse ndi abodza, ngakhale atachitidwa m'dzina la Yesu Khristu kapena m'dzina la Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera mwa kumizidwa m’madzi.
Kacou Philippe amawona Baibulo ngati galasi lowonera kumbuyo la galimoto kapena bukhu la mbiri. Kwa iye, Baibulo ndi chotsalira cha mbiri yakale ya chikhristu ndiponso chiyuda ndipo silingapereke moyo wosatha kwa njira iliyonse. Iye amawotcha mitundu yonse ya Baibulo yomwe iye akuitenga kukhala yoopsya kwa chikhulupiriro, chitsanzo cha Tob, King James, Tompson, Scofield ndiponso Louis Segond. Kacou Philippe akufotokozanso zomwe Mawu wa Mulungu ali, kulekanitsa pakati pa Mawu wa Mulungu (zoona zoululidwa) ndi theology (zidziwitso zopezedwa kudzera mu luntha). Iye akufotokozanso umulungu wa Yesu Khristu, kulapa kwa machimo kumene kuyenera kukhala kwa pagulu, malo wa mkazi mu Mpingo, ubatizo wa m'madzi, Mzimu Woyera, mneneri, Baibulo, ubale pakati pa Mpingo ndi Boma ndiponso zinthu zina zambiri za chikhristu. Pa nkhaniyi, iye akana kupita ku msonkhano wa Ntchito Zazikulu za Zofufuzafufuza za ku Ivory Coast. Iye akufotokozanso chikhristu chonse mu ntchito yotchedwa Buku la mneneri Kacou Philippe, lofalitsidwa mu magawo atatu ndi Macope wa Édilivre ku France. Wonani nyuzipepala: Le Jour Plus N°3399 ya 15 epulo wa 2016 ndiponso nyuzipepala Le Sursaut N° ya 15 epulo wa 2016.
Mu Maritch wa 2008, Kacou Philippe asonkhanitsa gulu lonse la chipembedzo, komanso atolankhani ndiponso wanthu a m’magulu a wanthu, pa msonkhano wokhudza chikhristu. Ndiyo dondomeko yotsutsa mipingo. Nyuzipepala ina inena kuti iye ndi mtsogoleri wa mawu wa Mulungu. Padali pambuyo pa msonkhano umenewu pamene iye adawoneka patsamba loyamba la nyuzipepala ina: Mneneri wina avula anthu wa Mulungu. Monga William Branham, Kacou Philippe afotokoza kupezeka Kwa chawuzimu komwe iye amakutenga kukhala mngelo wa 24 epulo 1993.
Mu 2008, maulaliki wa Kacou Philippe ayamba kutanthauziridwa m’mzinenero zina. Nyuzipepala zikufalitsa maulaliki wake mwathunthu; ngakhale kuchokera kunja kwa Ivory Coast. Nyuzipepala ina yaku Cameroon ikufalitsa mu mutu wake wachikuto: Kacou Philippe, mneneri amene wabwera kudzakonzanso chikhristu. Mmakanema, monga Africa nº 1, zokambirana ziyambika. Anthu wena amayankha m’njira yachinsinsi, pomwe wena amapanga m’njira zowonekera komanso zachiwawa. Wenanso amapita patali kwambiri, akumatenganso ziphunzitso za Kacou Philippe chibodzi ndi chimodzi, ncholinga chakuti azithetse bwino.
Pa 13 meyi wa 2016, mneneri Kacou Philippe adamangidwa kunyumba kwake ndi akuluakulu wa boma wa Ivory Coast chifukwa chotsutsa ulamuliro wa boma, kusonkhezera udani wachipembedzo, ndiponso kuwopsyeza chipembedzo. Iye apanga masiku anayi ndi usana unayi atakhala pampando mu malo wa Luntha Lalikulu la ku Ivory Coast. Kenako iye apanga usana uwiri ndi usiku uwiri m'chipinda chapansi pa likulu la apolisi ku Abidjan ndiponso miyezi itatu ku ndende yaikulu ya Abidjan, asadapezenso ufulu wake usiku wa 16 ogasiti 2016 ndi kulandidwa ufulu wake wachibadwidwe, makamaka kuletsedwa kulalikira Uthenga Wabwino kwa zaka zisanu. Atolankhani a ku Togo ndiponso ku Cameroon afotokoza kuti mlanduwu ndi wosamveka.
Pambuyo pake, atsogoleri achipembedzo a ku Ivory Coast adavomereza kuti ndiwo adayambitsa
kugwidwa ndi kumangidwa kwake.
Kwa Kacou Philippe, utumiki wake wa mneneri uli ndi magawo awiri aakulu kapena kudziwika.
Gawo loyamba limene likadakhala ngati cholowa chomwe iye adalandira kwa bambo wake William Marrion Branham, chomwe ndicho chikwaniritso cha Mateyu 25:6 ndipo kuti ndiko kuphatikizika kwa mavumbulutso wake womwe ali kuchokera mu chaputala 1 mpaka chaputala 154 cha bukhu lake lotchedwa Buku la Mneneri Kacou Philippe. Ndipo gawo lachiwiri lomwe ndilo uneneri, maloto ndiponso masomphenya, lomwe ndilo kuphatikizika kwa mavumbulutso wake womwe ali kuchokera chaputala 155 mpaka chaputala 162 cha bukhu lake. Ndipo kuchokera chaputala 163 mpaka chiwerengero chosakhazikika, pakadali pano, zomwe zikadakhala kusonkhanitsidwa kwa maumboni wa machiritso ndiponso zozizwitsa kutsimikizira utumiki wake kudzera mu mautumiki angapo wa machiritso m'mayiko angapo padziko lapansi mpaka kukwaniritsidwa kwa masomphenya wa bwalo lalikulu lamasewera womwe iye adali nawo mu 1993.
Malingana ndi Kacou Philippe, maloto ndiponso masomphenya ndizo chinenero chopatulika pakati pa milungu ndi wanthu, kuphatikizapo ndi Mulungu Wamkulu. Iye amayerekeza maloto ndiponso masomphenya ndi malamulo ndi zizindikiro zowolokera pa kuguba kwa anthu kupita kwa Mulungu; kumene kunyalanyaza loto kapena masomphenya ndiko kusalabadira Mulungu amene akukamba nanu. - Choncho, malingana ndi iye, ndiyo nkhani yomwe iyenera kukambidwa m’mipingo yonse ndiponso zipembedzo za dziko lonse kuti awonetse kufunika kwa maloto ndiponso masomphenya kwa wokhulupirira. Komabe, kutanthauzira maloto ndiponso masomphenya kukadayenera kuchitidwa ndi nzeru zambiri ndi kusamala kumbali ya mtsogoleri aliyense wachipembedzo. Chifukwa ndi mwa mphatso ya Mulungu momwe izi zikadayenera kuchitidwa.
Kacou Philippe awona, mu masomphenya wena wa pa 5 Juni 2022, mngelo akumupatsa buku lobiriwira ndikuwonetsa kuti apite ku South Africa. Pa nthawi yoyenera, iye akumvetsa kuti buku lobiriwira ndilo pasipoti ndipo kuti, pambuyo pa zaka zopitilira 20 za utumiki popanda kutulika ku Ivory Coast, Mulungu akumupatsa tsopano lamulo loti achite ulendo wa mishoni ndipo kuti akadayenera kuyamba ndi kupita ku South Africa kuti akatengenso mphatso ya machiritso yosiyidwa ndi William Branham. Kudzera m'maloto ndiponso masomphenya angapo, iye akumvetsa kuti ayenera kukonza mautumiki wa machiritso ndiponso zozizwitsa mwaulere. Mngelo amulangiza mu 2021 kuti asalandire ndalama kapena mphotho iliyonse kuchokera kwa aliyense, mwa chifukwa chilichonse, pa nthawi ya utumiki wake wa machiritso. Iye akuyamba ndi mautumiki wake woyamba wa machiritso ku South Africa mu mwezi wa maritchi 2025 m'mizinda ingapo, makamaka Johannesburg ndi Pretoria, Middelburg, Zebediela ndipo mu mwezi wa epulo wa 2025 ku Zimbabwe, pambuyo pa kupeza mavuto wochepa pakulandira chiphaso choyendera. Mautumiki wa machiritso ku Zimbabwe adachitikira m'mizinda ya Harare ndi Bulawayo kuyambira pa 16 mpaka pa 21 epulo 2025. Wodwala angapo, akhungu, wofa ziwalo, wopunduka, ndi HIV, wogontha, adachiritsidwa nthawi yomweyo kapena m’masiku angapo pambuyo, malingana ndi maumboni angapo. Atolankhani ambiri a ku South Africa, Zimbabwe, Ivory Coast, Benin, Cameroon, Central Africa ndiponso nyuzipepala zikuluzikulu monga Herald ndi Chronicle, adakamba za ulendo wa mneneri Kacou Philippe ku South Africa ndiponso ku Zimbabwe. -Malingana ndi Kacou Philippe, ulendo wake wa utumiki ku South Africa ndipo, kenako, ku Zimbabwe, komanso zodabwitsa zake, ndi zolingana ndi za William Branham m'nthawi yake, mu 1951. Kulingana uku kwa zodabwitsa kukhoza kuwonedwa pambuyo powerenga kapena kumvetsera machaputala 163 ndi 164 wa bukhu la mneneri Kacou Philippe komanso bukhu la maumboni wovomerezeka wa William Branham, mneneri ayendera South Africa, wochokera kwa Julius Stadsklev. Ndipo kulingana uku kukadapereka chomaliza choonetsa kuti mngelo wa mtsinje wa Ohio ndiye mngelo yemweyo amene ali ndi mneneri Kacou Philippe. Pambuyo pa Zimbabwe, Kacou Philippe akadayenera kupita ku Gabon mu June wa 2025, koma Boma la Gabon lidamukaniza chiphaso choyendera chifukwa cha atsogoleri achipembedzo womwe akuwonetsa kutsutsa mautumiki wa machiritso aulere wa mneneri Kacou Philippe mwa zifukwa zingapo, koma makamaka chifukwa cha mtundu waulere kwathunthu wa mautumiki wa machiritso wa mneneri Kacou Philippe potsatira langizo lolimba la mngelo mu masomphenya mu 2021. Izi zidayambitsa kuthetsedwa kwa pulogalamu yake ku Gabon komanso mapulogalamu m'mayiko wena, monga Benin, Togo, Cameroon, Congo-Brazzaville ndiponso Congo-Kinshasa.
Zotanthauziridwa kuchokera ku https://plus.wikimonde.com/wiki/Kacou_Philippe